Gwanda Chakuamba
Gwandaguluwe Chakuamba Phiri amene anabadwa 1935, ndi munthu wina wotchuka pa nkhani ya ndale mu dziko la Malawi. Iwo amachokera ku chigwa cha mtsinje wa Shire kummwera kwa dzikoli. Anthu ambiri amaatchula kuti a Gwanda Chakuamba.
Zaka zoyambilira
SinthaniPamene dziko la Malawi linakhala loyima palokha mu 1964 mpaka 1980, a Chakuamba anali munthu wodziwika mu chipani cha Malawi Congress Party (MCP), chipani chokhacho chomwe chinali chololedwa mzikoli. Pa nthawi yomwe a Hastings Kamuzu Banda ankalamulira dziko la Malawi, a Chakuamba anakhala mu mipando yosiyana siyana mu chipanichi. Mpando wina unali mtsogoleri wa bungwe la a chinyamata la Malawi Young Pioneers (MYP). Mu 1980, iwo anapezeka wolakwa pa mulandu wotsutsa boma ndipo anamangidwa kwa zaka 22.
Ndale za zipani zambiri
SinthaniA Chakuamba anamasulidwa mwezi wa Julaye 1993 patangotha mwezi umodzi anthu a dzikoli atabvomera kuti mu dzikoli mukhale boma la zpani zambiri. Iwo atamasulidwa, analowa chipani cha United Democratic Front (UDF) koma patangopita ka nthawi kochepa, anabweleranso ku MCP ndipo anakhala Mulembi Wamkulu wa chipanichi. Mu Febuluale 1994, chipani cha MCP chinalengeza kuti Hastings Kamuzu Banda adzaimira chipanichi pa chisankho cha zipani zambiri choyamba cha mu dzikoli ndipo a Chakuamba adzaimira ngati wachiwiri wawo.
Pa chisankhochi, chomwe chinachitika pa 17 May 1994, a Bakili Muluzi ndi chipani chawo cha UDF anapambana ndipo a Banda ansiya ndale. Pa nthawi imeneyi, a Chakuamba anakhala mtsogoleri wa MCP. Mwezi wa Febuluale 1999, chipani cha MCP chinapanga mgiwirizano ndi chipani cha Alliance for Democracy (AFORD} ngati mbali ina yokhonzekera chisankho chomwe chinachitika mu Meyi chaka chomwecho. A Chakuamba anasankhidwa ngati mstogoleri wa mgwirizanowo ndipo a Chakufwa Chihana, mtsogoleri wa AFORD ngati wachiwiri wawo. Anthu otsatira MCP ambiri sanagwirizane nazo zimenezi chifukwa a Chakuamba sanasankhe a John Tembo kukhala wachiwiri wawo ndipo anayamba matukutuku ofuna kuti a Chakuamba atule pansi udindo wa utsogoleri wa chipanichi.
Pa chisankho chomwe chinachitika pa 15 Juni 1999, a Muluzi anapambananso ndipo a Chakuamba anali otsatira ndi 45% ya mavoti onse. Ngakhale odzawonelera chisankho ochokera ku maiko a kunja ananena kutu chisankhochi chinayenda mwa chilungamol, mgwirizano wa MCP ndi AFORD unakasuma ku bwalo la milandu potsutsana ndi zotsatira za chisankhochi ndipo anadandaula kuti panali chinyengo mu maboma 16. Bwaloli linapeza kuti panalibe chinyengo.
Mwezi wa Okotobala 2002, a Chakuamba anamangidwa kwa kanthawi kochepa chifukwa cholemba kalata ya bodza mu dzina la a Bakili Muluzi kwa aphungu a nyumba ya malamulo yonena kuti adzawapatsa ndalama akabvomera kuti a Muluzi adzaimenso kachitatu pa chisankho cha utsogoleri ngakhale malamulo a dzikoli samawalola kutero.
Pa miyezi yoyandikira chisankho cha 2004, a Chakuamba anasiya chipani cha MCP ndipo anayambitsa chipani chawo cha Republican Party (RP). Chipanichi chinapanga ubale ndi zipani zina zisanu ndi chimodzi ndi kupanga Mgwirizano Coalition. A Chakuamba anasankhidwa kukhala wotsogolera mgwirizanowo komanso kuti adzaimire gululi pa chisankho. Zotsatira za chisankho zonawonetsa a Chakuamba kuti anali wachitatu pa chisankhochi pambuyo pa a Bingu wa Muntharika wa UDF ndi a John Tembo a MCP, ndi 26% ya voti. the MCP, winning 25.7% of the vote. Kuwelenga kwa mavoti kusanathe, a Chakuamba analengeza kuti anapambana ndipo zotsatira zoonetsa kuti a Muntharika akutsogola zinali za bodza. A Muntharika anapambanabe ndipo analumbiritsidwa utsogoleri pa 24 Meyi ngakhale a Chakuamba ankanena kuti zotsatirazosinali zobera.
Kumayambiliro a mwezi wa Juni, a Chakuamba anasiya kutsutsa zotsatira za chisankhochi ndipo analola kuthandiza boma la a Muntharika. Iwo sanapatsidwe unduna koma anthu ena atatu a chipani chawo cha RP anapatsidwa mipando mbomali. A Chakuamba anapatsidwa unduna wa zaulimu mu Febuluale 2005, ndipo anasiya chipani cha RP ndikukalowa DPP. Iwo anasankhidwa kukhala woyamba wa wachiwiri wa mstogoleri wa dziko. Mu Sepitembala 2005 a Chakuamba anachotsedwa unduna ndipo anafundidwa ndi apolisi patangopita masiku ochepa chifukwa chonena kuti a Muntharika akhala atachoka pa udindo pasanafike pa Khilisimasi.