John Tembo
John Zenasi Ungapake Tembo, amene anabadwa pa 14 Sepitembala 1932 ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) cha mudziko la Malawi chomwe chili chipani chachikulu chotsutsa mu dzikoli. A Tembo amachokera m’boma la Dedza ndipo ndi mphunzitsi.[1]
Moyo wawo wakale
SinthaniA Tembo anasankhidwa kukhala mmodzi wa aphungu a nyumba ya Nyasaland (dzina la kale la dziko la Malawi) mu 1961, zaka zitatu dzikoli lisanalandire ufulu wodzilamulira lokha. Iwo anali munthu wachiwiri amene anakhala nduna ya zachuma mdzikoli atachoka a Sir Henry Phillips, mpando umene ankafuna kuti akhalepo a Dunduzu Chisiza. (A Chisiza anamwalira mu 1962 pa ngozi ya galimoto imene anthi ena amanena kuti siinali ngozi koma anthu anachita kupangitsa ndipo a Tembo amatchuka kuti ndi amene anapangitsa ngoziyi). A Tembo anali nduna yokhayo imene siintule pansi pamene nduna zina zinachotsedwa kapena kuthawa mdzikoli. Nthawi imeneyi, anthu ambiri amene amatsutsana ndi a Kamuzu Banda, amene anali mtsogoleri wa dziko la Malawi anathawa .
Ubale ndi a Kamuzu Banda
SinthaniA Tembo anali amene amaoneka kuti a Hastings Kamuzu Banda, mtsogoleri wa dziko la Malawi, ankawakhulupirlira kwambiri. Ubwenzi wawo unalimbikitsidwa pamene a Cecilia Tamanda Kadzamira, mwana wa a chemwali awo a a Tembo, anamutenga kukhala wothandizira a Banda, ndipo a Kadzamirawa amatchulidwanso kuti ‘Mama’. Chifukwa chakuti a Banda ankawakhulupilira ngati mlangizi, a Tembo anali ndi mphamvu zambiri pa nkhani ya ndale za dzikoli pa zaka zonse zomwe a Banda anli mtsogoleri. Mphamvu za a Tembo zinkawoneka ngati zimachulukira pemene a Banda anayamba kufooka chifukwa cha ukalamba. Zinali zodabwitsa kuti a Banda anasankha wina amene amatsutsana ndi a Tembo, a Gwanda Chakuamba kuti akhale wachiwiri wawo pamene kunachitika chisankho cha zipani zambiri mu 1994.
Mu 1995 chipani cha MCP chitalephera pa chisankhochi, a Tembo, ‘Mama’ komanso a Kamuzu Banda anazengedwa mulandu wokhudza kuphedwa kwa anthi ena otchuka pa ndale mu 1983 omwe amawaganizira kuti amadziwapo kanthu pa nkhaniyi. Mulanduwu umatchuka ndi dzina loti Mwanza Trial. Pamene palibe chikaiko chilichonse chakuti anthuwa anachita kuphedwa pa ngozi ya galimoto yomwe inachitika ku Mwanza mmanja mwa anthu oona a chitetezo a dzikoli, panalibe umboni weni weni wakuti a Tembo anatengapo mbali pa nkhaniyi ndipo iwo anapambana pa mulanduwo.
A Banda atamwalira 1997, a Tembo anayesa kulanda utsogoleri wa MCP kuchokera kwa a Chakuamba ndipo sanamvere chigamulo cha bwalo la milandu chowaletsa kuti asatero.Chifukwa cha ichi, iwo anachotsedwa mu nyumba ya malamulo. Ngakhale zinali choncho, a Tembo anakatsutsa nkhaniyi ku bwalo la milandu ndipo anabwezeredwa kukhalanso phungu wa nyumba ya malamulo. Panakali pano, iwo ndi Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma mu nyumbayi. Tembo anali munthu oyipa.
Chisankho cha 2004
SinthaniNgati woyimira chipani cha MCP mu 2004, a Tembo anali wachiwiri pa chisankho cha 2004 ndipo anapeza 27% ya mavoti onse. Iwo anali pambuyo pa a Bingu wa Muntharika amene ankayimira chipani cha United Democratic Front (UDF) ndiponso a Gwanda Chakuamba amene ankayimira Mgwirizano Coalition. Anthu ena oona za ndale amaganiza kuti a Tembo ali ndi mwayi wopambana pa chisankho chomwe chidzachitike mu dzikoli mu 2009.