Open main menu

Wikipedia β

A Elesoni Bakili Muluzi, amene anabadwa pa 17 Malichi 1943 anali mtsogoleri wa dziko la Malawi kuyambira 1994 mpaka 2004.

Moyo wawo wakaleEdit

A Muluzi anabadwira mmboma la Mangochi ndipo anagwirako ntchito mmboma. A Muluzi anakhala mmaudindo wosiyana siyana mu chipani cha Malawi Congress Party chomwe chinkalamulira dzikoli.

Utsogoleri wa dziko la MalawiEdit

Lernt schreiben, amene ankayimira chipani cha United Democratic Front (UDF) anakhala mtsogoleri wa dzikoli pamene anapambana pa chisankho cha utsogoleri cha zipani zambiri pomwe iwo anapambana ndi 47%. Iwowa anapeza ma voti ambiri kuposa mtsogoleri wa kale amene analamulira dzikoli kuyambira 1964, a Hastings Kamuzu Banda. A Muluzi anapambanso pa chisankho chomwe chinachitika mu 1999 popeza 52% ya mavoti onse, kuwaposa a Gwanda Chakuamba amene ankawoneka ngati apambana pa chisankhocho. Mu 2002, anthu owathandizira ankafuna kusintha malamulo akuti mtsogoleri aziyima pa chisankho kawiri kokha ndi cholinga chakuti a Muluzi ayime kachitatu. Maganizo amenewa anasiyidwa pamene anthu ena anatsutsana nalo ganizoli pochita ziwonetsero. Iwo anasiya boma mu mwezi wa Meyi 2004, ndipo amene anapambana chisankho anali a Bingu wa Muntharika amene ankayimiranso chipani cha UDF.


A Muluzi anali ndi maudindo muboma la a Hastings Kamuzu Banda koma iwo anali mmodzi mwa amene ankatsutsana ndi boma la chipani chimodzi. Ngakhale zinali chonchi, utsogoleri wa a Banda unali ndi nkhani zina zosakhala bwino, mwachitsanzo pamene iwo anagulitsa chimanga chomwe dzikoli linkasunga pa nthawi yomwe kunali njala komanso posokoneza ndalama zomwe zinapezeka pa malonda ndi maiko ena a chimangacho, ngakhale maiko ena akunja ankayesayesa kuti afufuze chomwe chinachitika. Anthu ambiri amaganiza kuti ndalamazi anagawana a Muluzi ndi wotsatira awo ndipo zinasungidwa ku nyumba zosungirako ndalama za maiko a kunja. Ngakhale kunali nkhani zambiri zotele, a Muluzi anali mtsogoleri wotchuka mu dzikolu makamaka ku madera a ku mmwela kwa dzikoli.

Moyo wawo atasiya utsogoleriEdit

Iwo anapitiliza kukhala mtsogoleri wa UDF ngakhale anasemphana maganizo ndi amene iwo anamusankha kukhala mtsogoleri, a Bingu wa Muntharika. A Muntharika anasiya chipani cha UDF ndikukapanga chipani chawo cha Democractic Progressive Party (DPP).


A Muluzi anamangidwa pa 27 Julaye 2006 pa milandu yokhudza ziphuphu koma anamasulidwa tsiku lomwelo. Patangopita ma ola ochepa, munthu amene ankafufuza za mulandu wa a Muluzi, a Gustav Kaliwo anaimitsidwa pa ntchito ndi a Muntharika. Pa chifukwa chimenechi, amene amazenga mulandu wa a Muluzi, a Ishmael Wadi anaimitsa mulanduwu.


Kuyambira mwezi wa Malichi 2007 anthu ena anayamba kunena kuti a Muluzi adzaimenso pa chisankho chomwe chidzachitike mu 2009 ndipo anawapatsa nthawi yakuti anene ngati ankafuna kudzaima pa chisankhocho. Pa 11 Malichi, a Muluzi analengeza kuti adzaimadi, ndipo otsatira awo ena ngati a Brown Mpinganjira komanso a Sam Mpasu, amene koyambilira ankafuna kudzaimira UDF pa chisankhochi, analengeza kuti sadzaima chifukwa cha chidwi chomwe a Muluzi anawonetsa kudzaima.


Ngakhale zili chonchi, pali kusamvetsetsa pa zomwe malamulo a dzikoli amanena zokhudza kuima pa chisankho cha atsogoleri akale chifukwa malamulowo amanena kuto mtsogoleri sangaime kachitatu kotsatizana ndipo a Muluzi akufuna kuima chifukwa sanaime pa chisankho chomwe chinachitika 2004. Pa chifukwa chimenechi, anthu ambiri akufuna kuti malamulowo asinthidwe ndipo kuti mawu onena zotsatizana achotsedwe mu malamulowo.