United Democratic Front

United Democtratic Front (UDF) ndi chipani cha ndale cha mu dziko la Malaŵi. Chipanichi ndi chotchuka ku mmwera kwa dzikoli ndipo chili ndi mphamvu kwambiri mmadera kumene kumakhala aYao. Chipanichi chinalembetsedwa ku bungwe la Liberal International, limene lili bungwe lomwe la zipani zomwe zimakhulupilira za ufulu wa munthu aliyense.

Mtsogoleri wa chipanichi ndi a Bakili Muluzi, amene anali mtsogoleri wa dziko la Malaŵi kuyambira 1994 mpaka 2004. Kuyambira mu chaka cha 2005, a Muluzi ndi wamkulu kwambiri wa chipanichi.

Amene anasankhidwa kuti ayimire chipanichi pa chisankho cha 2004, a Bingu wa Muntharika anapambana chisankhocho ndi 35.9% ya mavoti onse amene anaponyedwa. Chipanichi chinatenganso mipando 49 ya mipando 194 ya amphungu a nyumba ya malamulo. Chifukwa cha kusagwirizana ndi chipanichi ndi a Muluzi, makamaka ku mbali ya nkhani yolandira ziphuphu imene a Muluzi ankakhudzidwa nayo, a Muntharika anasiya chipanichi mu February 2005 ndipo anayambitsa chipani chawo cha Democratic Progressive Party (DPP).