Chilankhulo cha Chichewa

Chilankhula chi chichewa cha Ku Zambia ndi Malawi
(Redirected from Chicheŵa)

Chichewa, (Chicheŵa mu chilankhulo cha ku Malaŵi, chomwe chimatchulidwanso kuti Chinyanja) ndi chilankhulo cha anthu a chi Bantu ndipo chimalankhulidwa kwambiri kummwela kwa dziko la Malawi, ndi kumvuma kwa dziko la Zambia. Mau oyamba okuti Chi- amene amalembedwanso kuti Ci- amatanthauza “mokhala ngati”, motero liu loti Chichewa limatanthauza “mokhala ngati Achewa”, choncho chilankhulochi chimadziwikanso ndi maina okuti Chewa kapena Nyanja. Chingoni (Ngoni) ndi Chikunda (Kunda) ndi kalankhulidwe kena ka chilankhulochi. Ena mwa ma Liu a mchichewa afanananso ndi Shona, isizulu ndebele komanso Isixhosa.

Kufala kwa Chilankhulochi

Sinthani

Chichewa ndi chimodzi mwa zilankhulo ziwiri zovomelezeka za dziko la Malawi (chilankhulo chinacho ndi Chingerezi), ndipo Chinyanja ndi chimodzi cha zilankhulo zisanu ndi ziwiri za dziko la Zambia, kumene chimalankhulidwa kwambiri kumvuma kwa dzikoli. Chichewa chimalankhulidwanso ku Mozambique, Maka maka mdera la Tete ndi Niassa ndiponso ku Zimbabwe kumene, malinga ndi kafukufuku, ndi chilankhulo chachitatu pa zilankhulo zonse za dzikolo, pambuyo pa Chishona ndi Chindebele. Maiko a Malawi, Zambia ndi Mozambique ndi kumene chilankhulochi chimayankhulidwa kwambiri. Baibulo ndi Khorani anatanthauziridwa mu Chichewa.

Zitsanzo zazitsanzo

Sinthani
Chingerezi Chewa (Malawi)[1] Town Nyanja (Lusaka)[2]
How are you? Muli bwanji? Muli bwanji?
I'm fine Ndili bwino Nili bwino / Niliche mushe
Thank you Zikomo Zikomo
Yes Inde Ee
No Iyayi/Ayi Iyayi
What's your name? Dzina lanu ndani?[3] Zina yanu ndimwe bandani?
My name is... Dzina langa ndine... Zina yanga ndine...
How many children do you have? Muli ndi ana angati? Muli na bana bangati?
I have two children Ndili ndi ana awiri Nili na bana babili
I want... Ndikufuna... Nifuna...
Food Chakudya Vakudya
Water Madzi Manzi
How much is it? Ndi zingati? Ni zingati?
See you tomorrow Tionana mawa Tizaonana mailo
I love you Ndimakukonda Nikukonda

Chichewa chinayambira ku ufumu wa Amaravi, umene unali wotchuka pa zaka za pakati pa 1500 ndi 1800. Ufumuwu unali ku Malawi, Zambia ndi Mozambique. Chilankhulochi chinakhalabe chotchuka ngakhale Angoni anagwetsa ufumu wa chi Maraviwo ndipo chinabvomerezedwa ndi ofalitsa uthenga wa Chikhristu pachiyambi pa chitsamunda. Ku Zambia, chilankhulochi chimatchuka ndi dzina lakuti Chinyanja, lomwe limatanthauza “chilankhulo cha Anyanja”, ndipo chimalankhulidwa ndi anthu a Chingoni ndi Chikunda. Mbali la Baibulo linatanthauziridwa mu chilankhulochi mu zaka za m’ma 1900.

Zolemba

Sinthani
  1. Paas (2016).
  2. Mitu ya Grey et al. (2013).
  3. Maxson (2011), p. 112.