True Jesus Church
"True Jesus Church" ndi mpingo woima pa okha, womwe udakhazikitsidwa ku Beijing, China, m'chaka cha 1917. Lero uli ndi anthu opembedza pafupifupi milioni imodzi ndi theka m'maiko makumi anayi ndi asanu (45), mu kontinenti zisanu ndi imodzi. Mpingowu uli mu nthambi ya Pentecostal ya chipembedzo cha chikhirisitu, yomwe inayambika koyamba kwa 20th century. Chalichili limatsata fundo ya Umodzi yomwe imaphunzitsidwa mu mpingo wa Pentecostal (Jesus-Name doctrine). Cholinga chachikulu cha mpingowu ndi kulalikila za uthenga wabwino wa ambuye Yesu kwa mafuko ndi mitundu yonse ya pa dziko la pansi, pokonzekera kubweranso kachiwili kwa Yesu. Zikhulupiliro ndi ngodya zomwe zamanga mpingo ndi:
- Mzimu Woyera (Eng. Holy Spirit) - Kulandila Mzumi Woyera, kumene kumaoneka ndi kulankhula malilime, ndi kumene kumatsimikiza kuti tili ndi mbali ku ufumu wa kumwamba.
- Ubatizo - Kubatizidwa mmadzi ndi chizindikilo cha kukhululukidwa ku machimo komanso kubadwanso mwa tsopano. Kubatizidwa kotele kumayenera kuchitika pa malo amene pamapezeka madzi a chilengedwe monga pa mtsinje, pa nyanja kapenanso kasupe. Mbatizi, amene analandila kale ubatizo wa madzi ndi wa Mzimu Woyera, ndi amene amabatiza anthu m'zina la Yesu Kristu. Aliyense wobatizidwa amayenera kumizidwiratu mmadzi atawerama mutu ndikuyang'ana nkhope yake pansi.
- Kutsuka mapazi - Dongosolo lotsuka mapazi a anthu limamulola munthu kukhala ndi mbali kwa Yesu Khristu. Limakumbutsanso kuti munthu ayenera kukhala ndi chikondi, chiyero, kudzichepetsa, kukhululuka komanso kugwira ntchito ya Mulungi. Aliyense amene anabatizidwa amayeneranso kutsukidwa mapazi ake mu dzina la Yesu Khiristu. Anthu amathanso kuloledwa kutsukana mapazi.
- Mgonero - Mgonero ndi dongosolo lokumbukira imfa ya Ambuye Yesu. Umatilora kuti tikhale ndi mbali pa imfa yake kuti tidzakhale ndi moyo wosatha ndi kudzutsidwa pa tsiku lomaliza. Dongosoloti limachitika pa nthawi ina iliyonse pafupi pafupi ndipo amagwiritsa ntchito mkate opanda chofufumitsa komanso madzi ochokera ku ma grapes okha basi.
- Tsiku la sabata - Lasabata ndi tsiku loyera, lodalitsika, ndikuyeletsedwa ndiMulungu. Tsikuli linapatulidwa kukumbukira chilengedwe ndi chipulumutso chaMulungu, ndichiyembekezo champumulo mumoyo uli nkudza.
- Yesu Khirisitu - Yesu Khirisitu, amene anali mau anasanduka thupi, anafa pamtanda kuti akapulumutse ochimwa, patsiku lachitatu anauka kwaakufa, nakwera kumwamba. Iye yekha ndiye mpulumutsi waanthu onse, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, Mulungu yekhayo woona.
- Buku Lopatulika (Baibulo) - Buku loyera, lokhala ndichipangano chakale ndichatsopano, linauzilidwa ndiMulungu,ndiloona, ndiponso muyeso wachikhalidwe chachikhristu.
- Chipulumutso (Eng. Salvation) - Chipulumutso chimadza ndichisomo chaMulungu mwa Chikhulupiriro. Akhristu ayenera kudalira Mzimu Woyera kuti akathe kuyenda muchiyero, kupereka ulemu kwaMulungu ndi kukonda anthu onse.
- Chalichi - Mpingo wokhazikitsidwa ndiAmbuye wathu Yesu Khristu, mwa Mzimu Woyera panthawi.
- Chilamulo chomaliza - Ambuye adzabweranso patsiku lomaliza kuchokera kumwamba kudzaweruza dziko lapansi.Woyera adzalandira moyo wosatha, wochimwa kuchionongeko nthawi zonse.