Malawi Young Pioneers (MYP)

Gulu la Malawi Young Pioneers ndi gulu la achinyamata limene linakhazikitsadwa ndi mtsogoleri woyamba wa dziko la malawi, ngati mbali imodzi yophunzitsa achinyamatawa maluso antchito zosiyana siyana. Koma mkati kati mwake mwagululi mumkaphunzitsidwaso ntchito zina zomwe sizinali zokomera ambili mdzikoli maka pa ndale. Anayamba kuphunzitsidwa zausilikali ( nkhondo). Motero panafika pakuti amkatumizidwa kumayiko akunja kukaphunzira izi. Kupatura apo ,analiso ndi zida ndi malo osungirako zidazi . Koma pamene anthu a Malawi anafuna zipani zambili, malo ngati awa omwe amasungirako zidawa anaonongedwa ndi asilikali adziko la Malawi pamene anthu ambili sanalifuneso gululi.