Cape Town
Cape Town ndi boma kapena mzinda mu dziko la South Africa. Cape Town imatchedwa Kaapstad mu chiyankhulo cha Afrikana ndiposa Ikapa mu chiyankhulo cha chiXhosa. Tawuniyi ndi yachiwiri mukuchuluka kwa chiwerengero cha anthu kutsatila Joni yomwe ili ndi anthu ambiri mu South Africa. Tawuniyi imatchedwa mother city or mayi wa matawuni ndipo ndi tawuni yayikulu mu chigawo cha Western Cape. Nyumba ya malamulo ya South Africa ilinso ku Cape town, koma matawuni ena ofunika kuyendetsa dziko ndi Pretoria komwe kuli prezidenti ndi maofesi oyendetsela dziko ndi Bloemfontein komwe kuli khoti lalikulu.
| |||
Tawuni ya Cape Town imadziwika ndi gombe lake, maonekedwe ake okongola chifukwa cha maluwa ndi zachilengedwe zimene zimapezeka kumeneko komanso phiri lalikulu lokongola lotchedwa Table Mountain.
Tawuniyi ndi yotchuka kwambiri pa zinthu zambiri monga zaluso lopanga zinthu. Tawuniyi inasankhidwa ndi New York Times komanso Daily Telegraph mu 2014 kukhala tawuni yopambana yomwe anthu angakayendeleko ndi kukawona zambiri. Mutawuniyi munachitikila maeewero achikho cha dziko lapansi a mpira wa rugby mu chaka cha 1995 ndiponso chikho cha dziko la pansi cha mpira wa miyendo mu chaka cha 2010.
- kukula kwa malo: 2,461 km²
- Kuchuluka kwa anthu: 3,740,026 (2011)
- Anthu malingana ndi mtundu (2011)
- Anthu akuda 15.8%
- Achikaladi 44.6%
- Indian/Asian 1.4%
- Achizungu 32.3%
- Ena 1.9%
- Chiyankhulo choyamba(2011)
- ChiAfrikana 22.7%
- ChiXhosa 2.7%
- Chingerezi 67.1%
- Zina 7.1%
Tawuni ya Cape Town yoyambilila inamangidwa ndi kampani ya Dutch East India Company (VOC) ngati malo operekera zofunika ku mabwato amene amapita kuzambwe kwa Africa komanso India. Jan Van Riebeeck wa kampani ya VOC anafika pa 6 apulo mu chaka cha 1652 ndipo anakhazikitsa malo oyamba okhalapo azungu mu South Africa. Kenaka tawuniyi inakhula kwambiri kuposa cholinga chomwe inayikhazikilitsila ndipo inakhala malo a zachuma komanso chikhalidwe kwa anthu ochoka ku ulaya.
Anthu oyambilila kukhala mudelali amakha ku maphanga a Peers ku fish Hoel muzaka zoposela 15, 000 kapena 12, 000 zapitazo. Padakali pano anthu amangodziwa zinthu zochepa za anthu amenewa chifukwa umboni woyamba wolembedwa umapezeka pa zomwe Bartolomeu Dias ananena mu chaka cha 1488. Iyeyu anali mzungu woyamba kufika kumalowa ndipo anatchula malowa "Cape of Storms" (Cabo das Tormentas). Koma malowa anatchulidwa dzina lina ndi John II of Portugal ngati "Cape of Good Hope" (Cabo da Boa Esperança) chifukwa cha chiyembekezo chimene chinalipo chopeza njira ya panyanja kukafika ku India. Vasco da gama analemba zowona malowa mu chaka cha 1497. Muchaka cha 1510, pankhondo ya Salt river, Francisco de Almeida ndi ankhondo ake anagonjetsedwa ndi Goringhaiqua, gulu lina la anthu chikhoekhoe mothandizidwa ndi ng'ombe. Muzaka za ma 16 chakuti, mabwato azungu amayima pa gombe la Table bay kupita ku India. Amachita malonda a fodya, kopa, ayiloni ndi anthu achikhoekhoe, kusinthana ndi nyama ndi zinthu zina zofunika.