Phiri la Mulanje ndi lodziwika kwambiri chifukwa cha maonekedwe ake wokongolo komanso njira zake zomwe ziri m’Phirimu zomwe ndi zochitsa kaso kwa iwo woyendamo. Ngakhale anthu ambiri wochokera kunja amabwera kudzakwera Phiri la Mulanje, koma ndi zomera ndi nyama zochepa zokha tikuzidziwa bwino za m’Phirimu. Apa tikuwona nyama zazing’onozing’ono zimene zimakhala m’tchire komanso m’mitengo ya m’nkhalango ya Phiri la Mulanje. Malo ambiri amene nyamazi zimapezeka chitetezo chawo chikuwopsezedwa ndipo tsogolo la nyamazi ndi lodetsa nkhawa.[1]

Phiri la Mulanje

Zolemba

Sinthani
  1. UNESCO World Heritage Committee, 38th Session, Doha: Decision : 38 COM 8B.18 Mount Mulanje Cultural Landscape (Malawi)