Katekisma wa Heidelberg

Katekisma wa Heidelberg [1] analembedwa mumzinda wa Heidelberg mopemphedwa ndi mtsogoleri wotchuka wotchedwa Frederick wachitatu wa m’chigawo cha Palatinate, dziko la German m’zaka za pakati pa 1559 ndi 1576. Iye anali Mfumu ndiponso mKhristu. Kotero anasankha Zacharius Ursinus wa zaka 28 za kubadwa amene anali mphunzitsi wa za Mau a Mulungu pa sukulu ya ukachenjede ya Heidelberg ndi Caspar Olevianus wa zaka 26 za kubadwa amene anali mlaliki wa ku nyumba ya mfumuyi, kuti alembe buku la katekisma lophunzitsira achinyamata ndi kuthandizira abusa ndiponso aphunzitsi m’sukulu.

Katekisma wa Heidelberg

Frederick anapeza upangiri wabwino ndi mgwirizano pa ntchito yolemba Katekismayi kuchokera ku gawo la sukulu ya ukachenjede lowona za maphunziro apamwamba. Katekisma wa Heidelberg analandiridwa ndi nthumwi za Msonkhano waukulu wa mpingo wa Sinodi umene unachitikira ku Heidelberg ndipo kenaka Katekismayi anasindikizidwa ku dziko la Germany ndi mawu otsogolera olembedwa ndi Frederick wachitatu, tsiku la 19 mwezi wa Januwale, m’chaka cha 1563. Kusindikizidwa kwa chiwiri ndi chitatu m’chiyankhulo cha ChiGermany, mawu ochepa ofotokozera pa funso lililonse analembedwa naphatikizidwa ndipo izinso zinakhala moteronso ndi Katekisma womasuliridwa m’chiLatini, m’chaka chomwecho. Mafunso ndi mayankho 129 a Katekismayi kenaka anagawidwa m’timagawo makumi asanu ndi mphambu ziwiri (52), kuti kagawo kalikonse kaphunzitsidwe m’mipingo sabata iliyonse pachaka.

  1. Zacharias Ursinus ndi Caspar Olevianus, Katekisma wa Heidelberg, Zomba, 2005