Blantyre
Blantyre ndi mzinda wina wa dziko la Malawi. Kwa nthawi yaitali, mzindawu unali likulu la za chuma ndi za malonda mdzikoli ngakhale likulu la dzikoli lili ku Lilongwe. Blantyre ndi mzinda wofunika kwa dziko la Malawi chifukwa ndi mzinda omwe kumapezeka malo ofunika ngati Malawi Polytechnic,yomwe ndi sukulu ya za ukachenjede ku malawi,sukulu zina za ukachenjede zomwe zili ku Blantyre ndi College of Medicine (Sukulu ya a dotolo),College of Health Sciences ndi likulu la Malawi college of Accountancy. Apa ndiye kuti tingathe kunena kuti Blantyre ndi likulu la za maphunziro a ukachenjede.