Adolf Hitler
Adolf Hitler anali mtsogoleri wa dziko la Germany kuyambira muzaka za 1934 mpakana 1945. Adolf analinso mtsogoleri wa chipani cha Nazi, ndipo anakhala Chancellor wa Germany mu chaka cha 1933 ndiponso Führer (fyula) mu chaka cha 1934. Muzaka zomwe iye anali mtsogoleri, anayambitsa nkhondo yachiwiri yadziko lonse pamene ankhondo ake analowa mu dziko la Poland pa 1 Seputembala mu chaka cha 1939. Iye anali akuyang'anila zonse zochitika munkhondoyi ndipo ndi amene anatsogolera kuti anthu achiyuda okwana 6 miliyoni aphedwe.
Hilter anabadwila ku Austria - ndipo anakulira kumalo apafupi ndi dera la Linz. Iye anapita ku Germany mu chaka cha 1913 ndipo analandila nyota chifukwa cha kuzipereka kwake pakumenya nkhondo mbali ya Germany mu nkhondo yoyamba yayikulu. Iye analowa chipani cha German Workers' Party (DAP) nkhondo itatha. Hilter anasankhidwa kukhala mtsogoleri wa chipani cha Nazi mu chaka cha 1921. Mu chaka cha 1923, iye anayesela kulanda boma la Germany mu mzinda wa Munich koma analephera ndipo anamagidwa ndikupasidwa zaka zisanu mundende. Ali mundende iye analemba buku lake la moyo wake lotchedwa Mein Kampf (kulimbana kwanga). Anatulutsidwa mu ndende mu chaka cha 1924. Hilter anapeza anthu omutsatila ambiri chifukwa chosagwirizana ndi mgwirizano wa Versailles, kukondera Germany yokha, kudana ndi anthu achiyuda ndi achikomunisti ndiponse kuyankhula kwake kwa mbalume ndi chikoka. Iye anamayankhula zambiri zokhuza chikomunisti kuti zinali zopangidwa ndi anthu achiyuda.
Hilter anakhazikitsidwa kukhala mtsogoleri wa Germany ndipo anapatsidwa mphamvu zonse kulamulila Germany mu chaka cha 1933. Iye anali ndi ganizo lothamangitsa Ayuda onse mu Germany. Mu zaka zoyambiira za ulamuliro wake Hilter anabweretsa chitukuko zimene zinapangitsa anthu ambiri ku Germany kumutsatila. Iye analandanso madela amene kumakhala anthu ena achiGerman mumayiko oyandikana nawo zomwe zinasangalatsa anthu ambiri. Iye anakhazikitsanso ntchito yopanga zida za nkhondo, ndege zomenyela nkhondo komanso sitima zapamadzi.
Ankhondo aku Germany analowa mu poland muchaka ch 1939 zimene zinapangitsa Britain ndi France kulowelera. Iye analamulanso ankhondo ake kulowa mu dziko la Soviet union. Kumapeto a chaka cha 1941, asilikali a Germany anali akalanda madela ambiri aku Ulaya komanso kumpoto kwa afrika. Koma zonsezi zinasintha mu chaka cha 1945 pamene asilikali a German anagonjetsedwa. Pa 29 Apulo mu chaka cha 1945, Hilter anakwatila chibwenzi chake cha nthawi yayitali Eva Braun ku Berlin atangokhala masiku ochepa kuti adziphe. Mumasiku awiri atangokwatilana, Hilter ndi mkazi wake anadzipha kuwopa kugwidwa ndi ankhondo aku Soviet omwe anali atafika kale mu mzinda wa Berlin. Matupi awo anawotchedwa.